APPEAL FOR SUBMISSION OF ANY RELEVANT INFORMATION AS REGARDS ALLEGATIONS OF NEGLIGENCE BY CENTRAL HOSPITALS RESULTING IN REMOVAL OF UTERUSES OF THE WOMEN UNDERGOING CAESAREAN SECTION.

In pursuance of its investigative powers conferred by section 123 the Office of the Ombudsman (the Office) is currently conducting Systemic Investigations into allegations of negligence in discharge of duty by personnel in the Central Hospitals. In particular, the allegation made is that there is mishandling of pregnant women undergoing caesarean section resulting in development of infections and ultimately removal of uteruses from these women most of whom are relatively young. The allegations emanate from a Zodiac Broadcasting Corporation report of August, 2018 which pointed out that there has been an increase in the number of uteruses removed with more than 20 uteruses allegedly removed in July 2018 alone at Queen Elizabeth Central Hospital.

In order to establish the veracity and the extent of the allegations the Office would like to get information from members of the public who have experienced the same fate directly or indirectly or indeed have any kind of information relating to this allegation. The Office is therefore appealing to all members of the general public with such information to kindly make submissions in written form which should be addressed to:

The Ombudsman, Private Bag 348, Lilongwe 3.

Alternatively, the submissions can be made through our facebook (Office of the Ombudsman-Malawi - https://www.facebook.com/ombudsmanmw) or twitter (Office of the Ombudsman@MWOmbuds) pages. Affected people can also send normal text messages or WhatsApp messages to the following numbers:

+265999263000/ +265991701747/ +265999317418

The submissions which should contain full names and contact phone numbers of those affected should be made by 20th December 2018.

KUPEMPHA UMBONI OKHUDZANA NDI NKHANI YOCHOTSEDWA CHIBEREKERO KAMBA KAKUSALABADIRIDWA NDI ANTHU OGWIRA NTCHITO KU CHIPATALA PANTHAWI YOMWE AZIMAYI AKUBEREKA KUDZERA MUNJIRA YA OPERESHONI

Pogwiritsa ntchito mphamvu zomwe Ofesi ya Ombudsman inapatsidwa kudzera m'malamulo a dziko lino sekishoni 123, ofesiyi ikuchita kafukufuku okhudza m'chitidwe olekelera kapena kunyozera m'magwiridwe atchito kwa anthu ogwira ntchito, makamaka m'zipatala zikuluzikulu m'dziko muno. Mwazina, m'chitidwe monga kusalabadira azimayi apakati akapita kuchipatala kukabereka kudzera munjira ya opareshoni zomwe zikumayambitsa matenda osiyanasiyana kapena kuchotsedwa chiberekero kumene, pamene anthu ambiri okhuzidwawa ndi amayi achichepere.

Nkhaniyi idadziwika kwambiri potsatira zomwe nyumba youlutsa mau ya Zodiak idaulutsa nkhani mu mwezi wa august 2018,yokhudza kuchotsedwa chiberekero kwa azimayi oposa 20 mwezi wa July okha mu 2018 pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth mu mzinda wa Blantyre.

Pofuna kupeza umboni weniweni okhudza nkhaniyi, Ofesi ya Ombudzimani ikupempha anthu amene anakumana ndi mavuto ngati amenewa kapena akudziwa wina amene zinamuchitikira kapena aliyense amene ali ndi uthenga okhuza nkhaniyi kuti awauze a ofesi ya Ombudzimani pa keyala iyi:

The Ombudsman, Private Bag 348 Lilongwe 3

Mukhonzanso kuimba foni,kapena kutumiza uthenga wa phone za mmanja (SMS) pa manambala awa: 0999 263 000 | 0991 701 747 | 0999 317 418 kapena kulemba pa tsamba la ofesiyi la facebook (https://www.facebook.com/ombudsmanmw) kapena tsamba la Twitter (Office of the Ombudsman@MWOmbuds).

Onensetsani kuti potumiza uthangawu ikani dzina lonse ndi nambala ya foni ya amene anakumana ndi mavuto ngati amenewa pasanafike pa 20 December 2018

Published by: henri Kachisi
published on: 2018-11-26 - 14:00:00