Ofesi Ya Mkulu Omva Madandaulo aanthu

Kuyitanitsa maumboni ndi madandaulo okhudza mchitidwe wosokoneza ndikugwiritsa ntchito mosayenera ndalama zamuthumba lachitukuko la mma khonsolo aboma

Ofesi ya mkulu omva madandaulo a anthu yakhala ikulandira madandaulo kuchokera kwa anthu, madera komanso mbali zosiyansiyana okhudza kagwilitsidwe ntchito kosayenera komanso kusakaza ndalama za thumba la chitukuko chakudera la aphungu (CDF), Thumba lachitukuko cha maboma aang’ono kapena khonsolo(LDF), Thumba la ntchito zachitukuko cha boma lonse (DDF) ndalama zachitukuko zoyang’aniridwa ndi eni dera (COMSEP), ndi ndalama zina zachitukuko mma khonsolo am’maboma. Potsatira mphamvu zimene ofesi ya mkulu omva madandaulo a anthu inapatsidwa ndi gawo 123 ya malamulo a dziko la Malawi, ofesiyi ikuyitanitsa aliyense amene ali ndi umboni omwe ungathandize pa kafukufukuyu kuti awadziwitse.

Zomwe tikufuna:

Anthu okhudzidwa (monga komiti zachitukuko za mmudzi (VDC), anthu wamba, Komiti zachitukuko zadera (ADC), Komiti zachitukuko zapaboma (DDC), mabungwe omwe si aboma, amipingo, opanga kafukufuku ndi ena onse) akupemphedwa kutumiza nkhani iliyonse yomwe ali nayo kapena kufotokoza zomwe anaona zokhudza kusakaza ndikugwiritsa ntchito mosayenera ndalama zamnthumba lachitukuko. Sizokhazi ayi, ofesiyi ikusakanso maumboni pankhani zakugwira ntchito molakwika izi:

  1. Kugwiritsa ntchito molakwika ndalama zamuthumba lachitukuko. Mwachitsanzo, pogwiritsa ndalama zathumbali pantchito zomwe sizinaikidwe mu ndondomeko yomwe inakonzedwa.
  2. Kuzengereza kutsatira ndondomeko zoyenera zogulira katundu waboma, Komanso kuphwanya ndodomeko zoyenera kutsatiridwa pogwira ntchito ya boma.
  3. Kuzengereza kuonetsetsa kuti katundu yemwe wagulidwa ndiwa kolite yabwino. Mwachitsanzo pogula katundu ndizipangizo zosalongosoka.
  4. Kuzengereza kugwira ntchito moyenera pogula katundu kapena kupeza ogwira ntchito omwe mitengo yawo ndiyodula kwambili kuposa mitengo yovomerezeka. Komanso kugula katundu yemwe masiku ake akutha ntchito anadutsa.
  5. Kukanika kulondoloza ndalama kapena katundu amene anagulidwa. Mwachitsanzo ndalama zagwiritsidwa ntchito koma ntchito yomwe imayenera kugwiridwa siinathe.
  6. Kukanika kukwaniritsa kutsatira ndondomeko zoyenera zokhudza ntchito yachitukuko (mwachitsanzo kusamaliza ntchito kapena kusakhutilitsa mlingo woyenera wantchito).
  7. Kusapereka tsatanetsatane wamomwe chitukuko chayendera kwa eni ake chitukuko ndi ku boma. Mwachitsanzo makhonsolo osapereka tsatanetsatane ku eni dera wa mmene ndalama zagwirira ntchito komanso katundu amene wagulidwa ndi ndalamazo.

Kutumiza madandaulowa

Madandaulo onse atumizidwe ku;

The Ombudsman,

Private Bag 348,

Lilongwe 3.

Or

ombudsman@ombudsmanmalawi.org

Komanso akhoza kutumiza uthengawu kudzera pa tsamba lathu la facebook (Office of the Ombudsman-Malawi – https://www.facebook.com/ombudsmanmw)  kapena tsamba la twitter (Office of the Ombudsman@MWOmbuds). Anthu onse amene akukhuzidwa angathenso kutumiza uthenga wa pa foni wa sms kapena whatsapp kumanambala awa:

Chigawo Chakummwera: +265 999 944 774

Chigawo Chakummawa: +265 996 053 267

Chigawo Chapakati: +265 881 101 571

Chigawo Chakumpoto: +265 999 317 418

Uthenga wanu ukhale ndi mayina onse ndi mafoni nambala a amene akukhuzidwa ndipo utumizidwe pofika pa 20th December 2019.  Ofesiyi ikutsimikira anthu onse kuti mayina awo ndi zonse zodziwikitsa anthu omwe atumize maumboni sizidzaululidwa ndipo madandaulo onse omwe atumizidwe adzasungidwa mwachisinsi komanso adzagwiritsidwa ntchito pothandizira kafukufukuyu basi.

 

Published by: henri kachisi
published on: 2019-10-17 - 10:26:08